Eksodo 34:24-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Pakuti ndidzaingitsa mitundu ya anthu pamaso pako, ndi kukulitsa malire ako; ndipo palibe munthu adzakhumba dziko lako, pakukwera iwe kudzaoneka pamaso pa Yehova Mulungu wako katatu caka cimodzi.

25. Usapereke mwazi wa nsembe yanga yophera pamodzi ndi mkate wacotupitsa; ndi nsembe yophera ya madyerero a Paskha asaisiye kufikira m'mawa.

26. Uzibwera nazo zipatso zoyambayamba za nthaka yako ku nyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphika mwana wa mbuzi mu mkaka wa mace.

27. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ulembere mau awa; pakuti monga mwa mau awa ndapangana ndi iwe ndi Israyeli.

28. Ndipo anakhala pomwepo ndi Yehova masiku makumi anai, usana ndi usiku; sanadya mkate kapena kumwa madzi. Ndipo analembera pa magomewo mau a panganolo, mau khumiwo.

29. Ndipo kunali pakutsika Mose pa phiri la Sinai, ndi magome awiri a mboni m'dzanja lace la Mose, pakutsika iye m'phirimo, Mose sanadziwa kuti khungu la nkhope yace linanyezimira popeza iye adalankhula naye.

30. Ndipo pamene Aroni ndi ana onse a Israyeli anaona Mose, taonani, khungu la nkhope yace linanyezimira; ndipo anaopa kumyandikiza.

31. Koma Mose anawaitana; ndipo Aroni ndi akazembe onse a khamu la anthu anabwera kwa iye; ndipo Mose analankhula nao.

32. Ndipo atatero, ana onse a Israyeli anayandikiza; ndipo iye anawauza zonse Yehova adalankhula naye m'phiri la Sinai.

Eksodo 34