23. Amuna ako onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israyeli, katatu caka cimodzi.
24. Pakuti ndidzaingitsa mitundu ya anthu pamaso pako, ndi kukulitsa malire ako; ndipo palibe munthu adzakhumba dziko lako, pakukwera iwe kudzaoneka pamaso pa Yehova Mulungu wako katatu caka cimodzi.
25. Usapereke mwazi wa nsembe yanga yophera pamodzi ndi mkate wacotupitsa; ndi nsembe yophera ya madyerero a Paskha asaisiye kufikira m'mawa.
26. Uzibwera nazo zipatso zoyambayamba za nthaka yako ku nyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphika mwana wa mbuzi mu mkaka wa mace.
27. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ulembere mau awa; pakuti monga mwa mau awa ndapangana ndi iwe ndi Israyeli.
28. Ndipo anakhala pomwepo ndi Yehova masiku makumi anai, usana ndi usiku; sanadya mkate kapena kumwa madzi. Ndipo analembera pa magomewo mau a panganolo, mau khumiwo.