2 Mbiri 21:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehosafati anagona pamodzi ndi makolo ace, naikidwa pamodzi ndi makolo ace m'mudzi wa Davide; ndi Yehoramu mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

2. Ndipo anali nao abale ace, ana a Yehosafati, Azariya, ndi Yehieli, ndi Zekariya, ndi Azariya, ndi Mikaeli, ndi Sefatiya, onsewa ndiwe ana a Yehosafati mfumu ya Israyeli.

3. Ndipo atate wao anawapatsa mphatso zazikuru, za siliva, ndi za golidi, ndi za mtengo wace, pamodzi ndi midzi yamalinga m'Yuda; koma ufumu anauninkha kwa Yehoramu; pakuti ndiye mwana wace woyamba.

4. Atauka tsono Yehoramu m'ufumu wa atate wace, nadzilimbitsa, anapha ndi lupanga abale ace onse, ndi akalonga ena omwe a Israyeli,

5. Yehoramu anali wa zaka makumi atatu mphambu ziwiri polowa ufumu wace, nacita ufumu m'Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu.

6. Nayenda m'njira ya mafumu a Israyeli, umo anacitira nyumba ya Ahabu; pakuti mwana wamkazi wa Ahabu anali mkazi wace; ndipo anacita coipa pamaso pa Yehova.

2 Mbiri 21