8. Ndipo kudzacitika tsiku la nsembe ya Yehova, kuti ndidzalanga akalonga ndi ana a mfumu, ndi onse akubvala cobvala cacilendo.
9. Ndipo tsiku ilo ndidzalanga olumpha ciundo, nadzaza nyumba ya mbuye wao ndi ciwawa ndi cinyengo.
10. Ndipo tsiku ilo, ati Yehova, kudzakhala phokoso lakulira locokera ku cipata cansomba, ndi kucema kocokera ku dera laciwiri, ndi kugamuka kwakukuru kocokera kuzitunda.
11. Cemani okhala m'cigwa, pakuti amalonda onse atayika, onsewo osenza siliva aonongeka.
12. Ndipo kudzacitika nthawi yomweyi kuti ndidzasanthula Yerusalemu ndi nyali, ndipo ndidzalanga amunawo okhala ndi nsenga, onena m'mtima mwao, Yehova sacita cokoma, kapena kucita coipa.