Yoswa 20:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova anati kwa Yoswa,

2. Nena ndi ana a Israyeli ndi kuti, Mudziikire midzi yopulumukirako, monga ndinanena kwa inu mwa dzanja la Mose,

3. kuti athawireko wakupha munthu osamupha dala, osadziwa; ndipo idzakhalira inu yopulumukirako, kumpulumuka wolipsa mwazi.

4. Munthu akathawira umodzi wa midzi iyi, aziima polowera pa cipata ca mudziwo, nafotokozere mlandu wace m'makutu a akuru a mudziwo; pamenepo azimlandira kumudzi kwao, ndi kumpatsa malo, kuti akhale pakati pao.

5. Ndipo akamlondola wolipsa mwazi, asampereke m'dzanja lace wakupha mnzaceyo; pakuti anakantha mnansi wace mosadziwa, osamuda kale.

6. Ndipo azikhala m'mudzimo mpaka adzaima pamaso pa msonkhano anene mlandu wace, mpaka atafa mkulu wansembe wa m'masiku omwewo; pamenepo wakupha mnzace azibwerera ndi kufika kumudzi kwace, ndi nyumba yace, kumudzi kumene adathawako.

7. Ndipo anapatula Kedesi m'Galileya ku mapiri a Nafitali, ndi Sekemu ku mapiri a Efraimu, ndi mudzi wa Ariba ndiwo Hebroni ku mapiri a Yuda.

Yoswa 20