49. Yesu anayankha, Ndiribe ciwanda Ine; koma ndilemekeza Atate wanga, ndipo inu mundipeputsa.
50. Koma 8 Ine sinditsata ulemerero wanga; alipo woutsata ndi wakuweruza.
51. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, 9 Munthu akasunga mau anga, sadzaona imfa nthawi yonse.
52. Ayuda anati kwa Iye, Tsopano tazindikira kuti muli ndi ciwanda. 10 Abrahamu anamwalira, ndi aneneri; ndipo Inu munena, Munthu akasunga mau anga, sadzalawa imfa ku nthawi yonse.
53. Kodi Inu ndinu wamkulu ndi atate wathu Abrahamu, amene anamwalira? ndipo aneneri anamwalira: mudziyesera nokha muli yani?
54. Yesu anayankha, Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemerero wanga uli cabe; 11 Atate wanga ndiye wondilemekeza Ine; amene munena za iye, kuti ndiye Mulungu wanu;
55. ndipo 12 inu simunamdziwa iye; koma Ine ndimdziwa iye; ndipo ngati ndinena kuti sindimdziwa iye, ndidzakhala wonama cimodzimodzi inu; koma ndimdziwa iye, ndipo ndisunga mau ace.