22. Zitapita in anadza Yesu ndi akuphunzira ace ku dziko la Yudeya; ndipo pamenepo anatsotsa nao pamodzi, nabatiza.
23. Ndipo Yohane analinkubatiza m'Ainoni pafupi pa Salemu, cifukwa panali madzi ambiri pamenepo; ndipo analinkufikako anthu, nalinkubatizidwa.
24. Pakuti Yohane sanaikidwe m'ndende.
25. Pamenepo padauka kufunsana mwa ophunzira ace a Yohane ndi Myuda za mayeretsedwe.
26. Ndipo anadza kwa Yohane, nati kwa iye, Rabi, Iye amene anali ndi inu tsidya lija la Y ordano, amene munamcitira umboni, taonani yemweyu abatiza, ndipo anthu onse alinkudza kwa iye.
27. Yohane anayankha nati, Munthu sakhoza kulandira kanthu, ngati sikapatsidwa kwa iye kocokera Kumwamba.