Yohane 10:10-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga, Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wocuruka.

11. Ine ndine Mbusa Wabwino; mbusa wabwino ataya moyo wace cifukwa ca nkhosa.

12. Wolipidwa amene sakhala mbusa, amene nkhosa siziri zace za yekha, aona mmbulu ulinkudza, nasiya nkhosazo, nathawa; ndipo mmbulu uzikwatula, nuzibalalitsa;

13. cifukwa ali wolipidwa, ndipo sasamala nkhosa.

14. Ine ndine Mbusa Wabwino; ndipo ndizindikira zanga, ndi zanga zindizindikira ine,

15. monga Atate andidziwa Ine, ndi Ine ndimdziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga cifukwa ca nkhosa.

16. Ndipo nkhosa zina ndiri nazo, zimene siziri za khola ili; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mau anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi,

17. Cifukwa ca ici Atate andikonda Ine, cifukwa nditaya Ine moyo wanga, kuti ndikautengenso,

Yohane 10