Yesaya 48:20-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Turukani inu m'Babulo, athaweni Akasidi; ndi mau akuyimba nenani inu, bukitsani ici, lalikirani ici, ngakhale ku malekezero a dziko; nenani, Yehova waombola mtumiki wace Yakobo.

21. Ndipo iwo sanamva ludzu, pamene Iye anawatsogolera m'mapululu; anawaturutsira madzi kuturuka m'matanthwe; anadulanso thanthwe, madzi nabulika.

22. 1 Kulibe mtendere, ati Yehova, kwa oipa.

Yesaya 48