18. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi cilungamo cako monga mafunde a nyanja;
19. mbeu yakonso ikadakhala monga mcenga ndi obadwa a m'cuuno mwako momwemo; dzina lace silikadacotsedwa, pena kuonongeka pamaso panga.
20. Turukani inu m'Babulo, athaweni Akasidi; ndi mau akuyimba nenani inu, bukitsani ici, lalikirani ici, ngakhale ku malekezero a dziko; nenani, Yehova waombola mtumiki wace Yakobo.
21. Ndipo iwo sanamva ludzu, pamene Iye anawatsogolera m'mapululu; anawaturutsira madzi kuturuka m'matanthwe; anadulanso thanthwe, madzi nabulika.
22. 1 Kulibe mtendere, ati Yehova, kwa oipa.