47. Cifukwa cace, taonani, masiku alinkudza, amene ndidzaweruza mafano osemasema a Babulo, ndipo dziko lace lonse lidzakhala ndi manyazi; ndipo ophedwa ace onse adzagwa pakati pace.
48. Pamenepo kumwamba ndi dziko lapansi, ndi zonse ziri m'menemo, zidzayimba mokondwerera Babulo; pakuti akufunkha adzafika kwa iye kucokera kumpoto, ati Yehova.
49. Monga Babulo wagwetsa ophedwa a Israyeli, momwemo pa Babulo padzagwa ophedwa a dziko lonse.
50. Inu amene mwapulumuka kulupanga, pitani inu, musaime ciimire; mukumbukire Yehova kutari, Yerusalemu alowe m'mtima mwanu.
51. Tiri ndi manyazi, cifukwa tamva mnyozo; manyazi aphimba nkhope zathu; pakuti alendo alowa m'malo opatulika a nyumba ya Yehova.
52. Cifukwa cace, taona, masiku alinkudza, ati Yehova, amene ndidzaweruza mafano ace; ndipo pa dziko lace lonse olasidwa adzabuula.
53. Ngakhale Babulo adzakwera kumwamba, ngakhale adzalimbitsa msanje wa mphamvu yace, koma kucokera kwa Ine akufunkha adzafika kwa iye, ati Yehova.
54. Mau akupfuula ocokera ku Babulo, ndi a cionongeko cacikuru ku dziko la Akasidi!