8. Ndipo panali, pamene Yeremiya anatha kunena mau onse amene Yehova anamuuza iye kuti anene kwa anthu onse, ansembe ndi aneneri ndi anthu onse anamgwira iye, ndi kuti, Udzafa ndithu.
9. Bwanji mwanenera m'dzina la Yehova, kuti, Nyumba iyi idzafanana ndi Silo, mudzi uwu udzakhala bwinja lopanda wokhalamo? Ndipo anthu onse anamsonkhanira Yeremiya m'nyumba ya Yehova.
10. Ndipo pamene akuru a Yuda anamva zimenezi, anakwera kuturuka ku nyumba ya mfumu kunka ku nyumba ya Yehova; ndipo anakhala pa khomo la cipata catsopano ca nyumba ya Yehova.
11. Ndipo ansembe ndi aneneri ananena kwa akuru ndi kwa anthu onse, kuti, Munthu uyu ayenera kufa; pakuti wanenera mudzi uwu monga mwamva ndi makutu anu.