Yeremiya 22:26-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndipo ndidzakuturutsa iwe, ndi mai wako wakubala iwe, kulowa m'dziko lina, limene sunabadwiramo; m'menemo udzafa.

27. Koma kudziko kumene moyo wao ukhumba kubwerera, kumeneko sadzabwerako.

28. Kodi munthu uyu Koniya ndiye mbiya yopepuka yosweka? Kodi ndiye mbiya yosakondweretsa? cifukwa canji aturutsidwa iye, ndi mbeu zace, ndi kuponyedwa m'dziko limene salidziwa?

Yeremiya 22