Yeremiya 10:14-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; woyenga yense anyazitsidwa ndi fanizo lace losemasema; pakuti fanizo lace loyenga liri bodza, mulibe mpweya mwa iwo.

15. Ndiwo cabe, ndiwo ciphamaso; pa nthawi ya kulangidwa kwao adzatha.

16. Gawo la Yakobo silifanana ndi iwo; pakuti iye ndiye analenga zonse; Israyeli ndiye mtundu wa colowa cace; dzina lace ndi Yehova wa makamu.

17. Nyamula katundu wako, iwe wokhala m'linga.

18. Pakuti atero Yehova, Taonani, ndidzaponya kunja okhala m'dziko ili tsopanoli, ndi kuwasautsa, kuti azindikire.

19. Tsoka ine, ndalaswa! bala langa lindipweteka; koma ine ndinati, Ndithu bvuto langa ndi ili, ndipirire nalo.

Yeremiya 10