2. Pamene dzanja la Midyani linalaka Israyeli, ana a Israyeli anadzikonzera ming'ang'ala ya m'mapiri, ndi mapanga, ndi malinga cifukwa ca Midyani.
3. Ndipo kunali, akabzala Israyeli, amakwera Amidyani, ndi Amaleki, ndi ana a kum'mawa, inde amawakwerera;
4. nawamangira misasa, namaononga zipatso za m'dziko mpaka ufika ku Gaza, osawasiyira cocirira njala m'Israyeli, ngakhale nkhosa, kapena ng'ombe, kapena buru.
5. Pakuti anakwera nazo zoweta zao ndi mahema ao, analowa ngati dzombe kucuruka kwao; iwowa ndi ngamila zao zomwe nzosawerengeka; ndipo analowa m'dziko kuliononga.
6. Ndipo Israyeli anafoka kwambiri cifukwa ca Midyani; ndipo ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova.
7. Ndipo kunali, pamene ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova cifukwa ca Midyani,
8. Yehova anatuma munthu mneneri kwa ana a Israyeli, nanena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Ine ndinakukwezani kucokera m'Aigupto, ndi kukuturutsani m'nyumba ya ukapolo;
9. ndipo ndinakulanditsani m'dzanja la Aaigupto, ndi m'dzanja la onse akupsinja inu, ndi kuwaingitsa pamaso panu, ndi kukupatsani dziko lao;
10. ndipo ndinati kwa inu, Ine ndine Yehova Mulungu wanu; musamaopa milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma simunamvera mau anga.
11. Pamenepo anadza mthenga wa Yehova, nakhala patsinde pa thundu wokhala m'Ofira, wa Yoasi M-abieziri; ndi mwana wace Gideoni analikuomba tirigu m'mopondera mphesa, awabisire Amidyani.
12. Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera, nati kwa iye, Yehova ali nawe, ngwazi iwe, wamphamvu iwe.
13. Ndipo Gideoni ananena naye, Mbuye wanga, ngati Yehova ali nafe catigwera ife bwanji conseci? ndipo ziti kuti zodabwiza zace zonse zimene makolo athu anatiwerengera, ndi kuti, Sanatikweza kodi Yehova kucokera m'Aigupto? Koma tsopano Yehova watitaya natipereka m'dzanja la Midyani.