28. Ndipo panalibe wolanditsa, popeza ku Sidoni nkutali, ndipo analibe kuyenderana ndi anthu ena; ndiko ku cigwa cokhala ku Betirehobo. Pamenepo anamanganso mudziwo, nakhala m'mwemo.
29. Ndipo analicha dzina la mudziwo Dani, kutsata dzina la atate wao Dani wombala Israyeli; koma poyambapo dzina la mudzi linali Laisi.
30. Ndipo ana a Dani anadziimitsira fane losemalo; ndi Yonatani mwana wa Gerisomu mwana wa Manase, iye ndi ana ace amuna anali ansembe a pfuko la Adani mpaka tsiku lija anatenga ndende anthu a m'dziko.
31. Motero anadziikira fane losema la Mika, limene adalipanga, masiku onse okhala nyumba ya Mulungu ku Silo.