Oweruza 11:36-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

36. Ndipo anati kwa iye, Atate wanga, mwamtsegulira Yehova pakamwa panu, mundicitire ine monga umo mudaturutsa mau pakamwa panu; popeza Yehova anakucitirani inu cilango pa adani anu, pa ana a Amoni.

37. Ndipo anati kwa atate wace, Andicitire ici, andileke miyezi iwiri, kuti ndicoke ndi kutsikira kumapiri, ndi kulirira unamwali wanga, ine ndi anzanga.

38. Nati iye, Muka. Namuuza amuke akakhale miyezi iwiri; namuka iye ndi anzace, nalirira unamwali wace pamapiri.

39. Ndipo kunali pakutha miyezi iwiri, anabwerera kwa atate wace amene anamcitira monga mwa cowinda cace anaciwinda; ndipo sanamdziwa mwamuna. Motero unali mwambo m'Israyeli,

40. kuti ana akazi a Israyeli akamuka caka ndi caka kumliririra mwana wa Yefita wa ku Gileadi, masiku anai pa caka.

Oweruza 11