Mateyu 3:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo masiku aja anadza Yohane Mbatizi, nalalikira m'cipululu ca Yudeya,

2. nanena, Tembenukani mitima; cifukwa Ufumu wa Kumwamba wayandikira.

3. Pakuti uyu ndiye ananenayo Yesaya mneneri, kuti,Mau a wopfuula m'cipululu,Konzani khwalala la Ambuye,Lungamitsani njira zace.

4. Ndipo Yohane yekhayo anali naco cobvala cace ca ubweya wangamila, ndi lamba lacikopa m'cuuno mwace; ndi cakudya cace cinali dzombe ndi uci wa kuthengo.

5. Pamenepo panamturukira iye ku Yerusalemu, ndi Yudeya lonse, ndi dziko lonse loyandikana ndi Yordano;

6. nabatizidwa ndi iye mu mtsinjewo wa Yordano, alikuulula macimo ao.

7. Ndipo iye pakuona ambiri a Afarisi ndi a Asaduki akudza ku ubatizo wace, anati kwa iwo, Obadwa a njoka inu, ndani anakulangizani kuthawa mkwiyo ulinkudza?

8. Onetsani inu zipatso zakuyenera kutembenuka mtima:

9. ndipo musamayesa kunena mwa inu nokha, Atate wathu tiri naye Abrahamu; pakuti ndinena kwa inu kuti mwa miyala iyi Mulungu akhoza kuukitsira Abrahamu ana.

10. Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo; cifukwa cace mtengo uli wonse wosabala zipatso zabwino udulidwa nuponyedwa pamoto,

11. Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zace: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:

12. couluzira cace ciri m'dzanja lace, ndipo adzayeretsa padwale pace; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wace m'ciruli, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima.

Mateyu 3