29. Ndipo onse amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda, cifukwa ca dzina langa, adzalandira zobwezeredwa zambirimbiri, nadzalowa moyo wosatha.
30. Koma ambiri oyamba adzakhala akuthungo, ndi akuthungo adzakhala oyamba.