Mateyu 10:27-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Cimene ndikuuzani inu mumdima, tacinenani poyera; ndi cimene mucimva m'khutu, mucilalikire pa macindwi nyumba.

28. Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe m'gehena.

29. Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu:

30. komatu inu, matsitsi onse a m'mutu mwanu awerengedwa.

31. Cifukwa cace musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri.

32. Cifukwa cace yense amene adzabvomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso nelidzambvomereza iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba.

33. Koma 1 yense amene adzandikana Ine pamaso pa anthu, Inenso nelidzamkana iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba.

34. 2 Musalingalire kuti nelidadzera kuponya mtendere pa dziko lapansi; sinelinadzera kuponya mtendere, koma lupanga.

35. 3 Pakuti ndinadza kusiyanitsa munthu ndi atate wace, ndi mwana wamkazi ndi amace, ndi mkazi wokwatiwa ndi mpongozi wace:

36. ndipo 4 apabanja ace a munthu adzakhala adani ace.

37. 5 Iye wakukonda atate wace, kapena amace koposa Ine, sayenera Ine, ndipo iye wakukonda mwana wace wamwamuna, kapena wamkazi koposa Ine, sayenera Ine.

38. Ndipo 6 iye amene satenga mtanda wace, natsata pambuyo panga, sayenera Ine.

39. 7 Iye amene apeza moyo wace, adzautaya; ndi iye amene ataya moyo wace, cifukwa ca Ine, adzaupeza.

40. 8 Iye wakulandira inu, andilandira Ine, ndi wakundilandira Ine, amlandira Iye amene ananditumiza Ine.

Mateyu 10