Mateyu 10:27-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Cimene ndikuuzani inu mumdima, tacinenani poyera; ndi cimene mucimva m'khutu, mucilalikire pa macindwi nyumba.

28. Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe m'gehena.

29. Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu:

30. komatu inu, matsitsi onse a m'mutu mwanu awerengedwa.

31. Cifukwa cace musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri.

32. Cifukwa cace yense amene adzabvomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso nelidzambvomereza iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba.

33. Koma 1 yense amene adzandikana Ine pamaso pa anthu, Inenso nelidzamkana iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba.

Mateyu 10