Masalmo 78:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Anakhazika mboni mwa Yakobo,Naika cilamulo mwa Israyeli,Ndizo analamulira atate athu,Akazidziwitse ana ao;

6. Kuti mbadwo ukudzawo udziwe, ndiwo ana amene akadzabadwa;Amene adzaimirira nadzafotokozera ana ao:

7. Ndi kuti ciyembekezo cao cikhale kwa Mulungu,Osaiwala zocita Mulungu,Koma kusunga malamulo ace ndiko.

8. Ndi kuti asange makolo ao,Ndiwo mbadwo woukirana ndi wopikisana ndi Mulungu;Mbadwo wosakonza mtima wao,Ndi mzimu wao sunakhazikika ndi Mulungu.

9. Ana a Efraimu okhala nazo zida, oponya nao mauta,Anabwerera m'mbuyo tsiku la nkhondo.

10. Sanasunga cipangano ca Mulungu,Nakana kuyenda m'cilamulo cace.

11. Ndipo anaiwala zocita Iye,Ndi zodabwiza zace zimene anawaonetsa.

Masalmo 78