Masalmo 59:14-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo abwere madzulo, auwe ngati garu,Nazungulire mudzi.

15. Ayendeyende ndi kufuna cakudya,Nacezere osakhuta.

16. Koma ine, ndidzayimbira mphamvu yanu;Inde ndidzayimbitsa cifundo canu mamawa:Pakuti Inu mwakhala msanje wanga,Ndi pothawirapo ine tsiku la nsautso yanga.

17. Ndidzayimbira zakukulemekezani Inu, mphamvu yanga:Pakuti Mulungu ndiye msanje wanga, Mulungu wa cifundo canga.

Masalmo 59