5. Ndipo anawafunsa, Muli nayo mikate ingati? Ndipo anati, Isanu ndi iwiri.
6. Ndipo analamulira anthu a khamulo akhale pansi; natenga mikate isanu ndi iwiriyo, nayamika, nanyema, napatsa ophunzira ace, kuti apereke kwa iwo; ndipo anapereka kwa khamulo.
7. Ndipo anali nato tinsomba towerengeka; ndipo Iye anatidalitsa, nati atipereke itonso.
8. Ndipo anadya nakhuta; ndipo anatola makombo malicero asanu ndi awiri.
9. Ndipo iwo anali ngati zikwi zinai; ndipo Iye analawirana nao.
10. Ndipo pomwepo analowa m'ngaiawa ndi akhupunzira ace, nafika ku mbali ya ku Dalmanuta.