5. Atero Ambuye Yehova kwa mafupa awa, Taonani, ndidzalonga mpweya mwa inu, ndipo mudzakhala ndi moyo.
6. Ndipo ndidzakuikirani mtsempha, ndi kufikitsira inu mnofu, ndi kukuta inu ndi khungu, ndi kulonga mpweya mwa inu; ndipo mudzakhala ndi moyo; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehoya.
7. M'mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndipo ponenera ine panali phokoso; ndipo taonani, panali gobede gobede, ndi mafupa anasendererana, pfupa kutsata pfupa linzace.
8. Ndipo ndinapenya, taonani, panali mitsempha pa iwo, panadzaponso mnofu, ndi khungu linawakuta pamwamba pace; koma munalibe mpweya mwa iwo.
9. Ndipo anati kwa ine, Nenera kwa mpweya, nenera, wobadwa ndi munthu iwe, nuti kwa mpweya, Atero Ambuye Yehova, Idza, mpweya iwe, kucokera ku mphepo zinai, nuuzire ophedwa awa, kuti akhale ndi moyo.