8. Koma anapandukira Ine, osafuna kundimvera Ine, sanataya yense zonyansa pamaso pace, sanaleka mafano a Aigupto; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'dziko la Aigupto.
9. Koma ndinacicita cifukwa ca dzina langa, kuti lisadetsedwe pamaso pa amitundu amene anakhala pakati pao, amene pamaso pao ndinadzidziwitsa kwa iwo, pakuwaturutsa m'dziko la Aigupto.
10. Momwemo ndinaturuka nao m'dziko la Aigupto, ndi kulowa nao kucipululu.
11. Ndinawapatsanso malemba anga, ndi kuwadziwitsa maweruzo anga, ndiwo munthu akawacita adzakhala nao ndi moyo.
12. Ndipo ndinawapatsanso masabata anga akhale cizindikilo pakati pa Ine ndi iwo, kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.
13. Koma nyumba ya Israyeli inapaodukira Ine m'cipululu, sanayenda m'malemba anga, nanyoza maweruzo anga, amene, munthu akawacita adzakhala nao ndi moyo; ndi masabata anga anawaipsa kwambiri; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga m'cipululu kuwatha.
14. Koma ndinacicita cifukwa ca dzina langa, kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu amene ndinawaturutsa pamaso pao.
15. Ndipo ndinawakwezeranso dzanja langa m'cipululu, kusawalowetsa m'dzikolo ndidawapatsa, moyenda mkaka ndi uci, ndilo lokometsetsa mwa maiko onse;
16. popeza ananyoza maweruzo anga, osayenda m'malemba anga, naipsa masabata anga; pakuti mitima yao inatsata mafano ao.
17. Koma diso langa lidawaleka osawaononga, sindinawatha onse m'cipululu.
18. Ndipo ndinati kwa ana ao m'cipululu, Musamayenda m'malemba a atate anu, musawasunga maweruzo ao, kapena kudzidetsa ndi mafano ao;
19. Ine ndine Yehova Mulungu wanu, muziyenda m'malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwacita;
20. muzipatulanso masabata anga, ndipo adzakhala cizindikilo pakati pa Ine ndi inu, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
21. Koma anawo anapandukira Ine, sanayenda m'malemba anga, kapena kusunga maweruzo anga kuwacita, amene munthu akawacita adzakhala nao ndi moyo; anaipsa masabata anga; pamenepo ndinati ndidzawatsanulira ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'cipululu.
22. Koma ndinabweza dzanja langa ndi kucicita, cifukwa ca dzina langa; kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu, amene ndinawaturutsa pamaso pao. Ndinawakwezeranso dzanja langa m'cipululu,
23. kuti ndidzawabalalitsa mwa amitundu, ndi kuwamwaza m'maiko;
24. popeza sanacita maweruzo anga, koma ananyoza malemba anga, naipsa masabata anga, ndi maso ao anatsata mafano a atate ao.
25. Momwemonso ndinawapatsa malemba amene sanali abwino, ndi maweruzo osakhala nao ndi moyo;