Ezara 5:8-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Adziwe mfumu kuti ife tinamuka ku dziko la Yuda, ku nyumba ya Mulungu wamkuru, yomangidwa ndi miyala yaikuru, niikidwa mitengo pamakoma, nicitika mofulumira nchitoyi, nikula m'dzanja mwao.

9. Pamenepo tinafunsa akulu aja ndi kutere nao, Anakulamulirani ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili?

10. Tinawafunsanso maina ao, kukudziwitsani, kuti tilembere maina a anthu akuwatsogolera.

11. Natiyankha mau motere, ndi kuti, Ife ndife akapolo a Mulungu wa Kumwamba ndi dziko lapansi, tirikumanga nyumba imene idamangika zapita zaka zambiri; inaimanga ndi kuitsiriza mfumu yaikuru ya Israyeli.

12. Koma makolo athuwo atautsa mkwiyo wa Mulungu wa Kumwamba, Iye anawapereka m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo Mkasidi, amene anaononga nyumba yino, natenga anthu ndende kumka nao ku Babulo.

13. Koma caka coyamba ca Koresi mfumu ya Babulo, Koresi mfumuyo analamulira kuti azimanga nyumba iyi ya Mulungu.

Ezara 5