Ezara 5:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo aneneri, Hagai mneneriyo, ndi Zekariya mwana wa Ido, ananenera kwa Ayuda okhala m'Yuda ndi m'Yerusalemu; m'dzina la Mulungu wa Israyeli ananenera kwa iwo.

2. Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealitiyeli, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ananyamuka, nayamba kumanga nyumba ya Mulungu iri ku Yerusalemu, anali pamodzi nao aneneri a Mulungu akuwathandiza.

3. Nthawi yomweyi anawadzera Tatinai kazembe tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setara Bozinai, ndi anzao, nanena nao motere, Anakulamulirani inu ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili?

Ezara 5