Deuteronomo 32:39-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

39. Tapenyani tsopano kuti Ine ndine iye,Ndipo palibe mulungu koma Ine;Ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi mayo:Ndikantha, ndicizanso Ine;Ndipo palibe wakulanditsa m'dzanja langa.

40. Pakuti ndikweza dzanja langa kuloza kumwamba,Ndipo nditi, Pali moyo wanga kosatha,

41. Ndikanola lupanga langa lonyezimira,Ndi dzanja langa likagwira ciweruzo;Ndidzabwezera cilango ondiukira,Ndi kulanga ondida.

42. Mibvi yanga ndiiledzeretsa nao mwazi,Ndi lupanga langa lidzalusira nyama;Ndi mwazi wa ophedwa ndi ogwidwa,Ndi mutu wacitsitsi wa mdani,

43. Kondwerani, amitundu inu, ndi anthu ace;Adzalipsira mwazi wa atumiki ace,Adzabwezera cilango akumuukira,Nadzafafanizira zoipa dziko lace, ndi anthu ace.

Deuteronomo 32