15. Abale, ndinena monga munthu Pangano, lingakhale la munthu, litalunzika, palibe munthu aliyesacabe, kapena kuonjezapo.
16. Ndipo malonjezano ananenedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yace, Sanena, Ndipo kwa zimbeu, ngati kunena zambiri; komatu ngati kunena imodzi, Ndipo kwa mbeu yako, ndiye Kristu.
17. Ndipo ici ndinena; Lamulo, limene linafika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi atatu, silifafaniza pangano lolunzika kale ndi Mulungu, kuliyesa lonjezanolo lacabe.
18. Pakuti ngati kulowa nyumba kucokera kulamulo, sikucokeranso kulonjezano; koma kumeneku Mulungu anampatsa Abrahamu kwaufulu mwa lonjezano.
19. Nanga cilamulo tsono? Cinaoniezeka cifukwa ca zolakwa, kufikira ikadza mbeu imene adailonjezera; ndipo cinakonzeka ndi angelo m'dzanja la Ilkhoswe.
20. Koma nkhoswe siiri ya mmodzi; koma Mulungu ali mmodzi.