8. mwa ana ao otsala m'dziko pambuyo pao, amene ana a Israyeli sanawatha, mwa iwowa Solomo anawacititsa thangata mpaka lero lino.
9. Koma mwa ana a Israyeli Solomo sanawayesa akapolo omgwirira nchito; koma iwowa anali anthu a nkhondo, akazembe ace akuru, ndi akuru a magareta ace, ndi apakavalo ace.
10. Amenewa anali akuru a akapitao a mfumu Solomo, ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu akulamulira anthu.
11. Ndipo Solomo anamkweretsa mwana wamkazi wa Farao m'mudzi wa Davide, alowe m'nyumba imene adammangira; pakuti anati, Mkazi wanga asakhale m'nyumba ya Davide mfumu ya Israyeli; popeza mpopatulika pamene panafika likasa la Yehova.