20. Ndipo kunacitika m'mawa, pomapereka nsembe yaufa, taonani, anafika madzi odzera ku Edomu; ndipo dziko linadzala ndi madzi.
21. Atamva tsono Amoabu onse kuti adakwera mafumu aja kuthirana nao nkhondo, anamemeza onse akumanga lamba m'cuuno ndi okulapo, naima iwo m'malire.
22. Ndipo pamene anauka mamawa dzuwa linawala pamadzipo, naona Amoabu madzi ali pandunji pao ali psyu ngati mwazi;
23. nati, Uja ndi mwazi, atha kuonongana mafumu aja, anakanthana wina ndi mnzace; ndipo tsopano, tiyeni Amoabu inu, tikafunkhe.
24. Ndipo pamene anafika ku misasa ya Israyeli, Aisrayeli ananyamuka, nakantha Amoabu, nathawa iwo pamaso pao; ndipo analowa m'dziko ndi kukantha Amoabu.