14. Koma Yesaya mneneri anadza kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Anatani anthu awa? anadza kwa inu kufumira kuti? Nati Hezekiya, Afumira dziko la kutari ku Babulo.
15. Nati iye, Anaona ciani m'nyumba mwanu? Nati Hezekiya, Zonse za m'nyumba mwanga anaziona, palibe kanthu pacuma canga kosawaonetsa.
16. Ndipo Yesaya anati kwa Hezekiya, Tamverani mau a Yehova.