32. Cifukwa cace atero Yehova za mfumu ya Asuri, iye sadzalowa m'mudzi muno, kapena kuponyamo mubvi, kapena kufikako ndi cikopa, kapena kuundira mtumbira.
33. Adzabwerera njira yomweyo anadzera, ndipo sadzalowa m'mudzi muno, ati Yehova.
34. Pakuti ndidzacinjiriza mudzi uno kuupulumutsa, cifukwa ca Ine mwini, ndi cifukwa ca Davide mtumiki wanga.