2 Mafumu 18:34-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

34. Iri kuti milungu ya Hamati, ndi ya Aripadi? iri kuti milungu ya Sefaravaimu, kapena Hena, ndi Iva? Kodi yalanditsa Samariya m'dzanja langa?

35. Ndi yiti mwa milungu yonse ya maiko inalanditsa maiko ao m'dzanja langa, kuti Yehova adzalanditsa Yerusalemu m'dzanja langa?

36. Koma anthuwo anakhala cete osamyankha mau; pakuti lamulo la mfumu ndilo kuti, Musamuyankha.

2 Mafumu 18