Zekariya 8:11-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Koma tsopano sindidzakhala kwa otsala a anthu awa monga momwe ndinakhalira masiku oyamba, ati Yehova wa makamu.

12. Pakuti padzakhala mbeu ya mtendere; mpesa udzapatsa zipatso zace, ndi nthaka idzapatsa zobala zace, ndi miyamba Idzapatsa mame ao; ndipo ndidzalandiritsa otsala a anthu awa izi zonse, cikhale colowa cao.

13. Ndipo kudzacitika kuti, monga munali cotembereretsa mwa amitundu, inu nyumba ya Yuda, ndi nyumba ya Israyeli, momwemo ndidzakusungani, ndipo mudzakhala codalitsa naco; musaope, alimbike manja anu.

14. Pakuti atero Yehova wa makamu: Monga ndil nalingirira kucitira inu coipa, muja makolo anu anautsa mkwiyo wanga, ati Yehova wa makamu, ndipo sindinawaleka;

15. momwemonso ndinalingirira masiku ano kucitira cokoma Yerusalemu ndi nyumba ya Yuda; musaopa.

16. Izi ndizo muzicite: Nenani coonadi yense ndi mnzace; weruzani zoona ndi ciweruzo ca mtendere m'zipata zanu;

Zekariya 8