1. Ndipo mau a Yehova wa makamui anadza kwa ine, ndi kuti,
2. Atero Yehova wa makamu: Ndimcitira nsanje Ziyoni ndi nsanje yaikuru, ndipo ndimcitira nsanje ndi ukali waukuru.
3. Atero Yehova: Ndabwerera kudza ku Ziyoni, ndidzakhala pakati pa Yerusalemu; ndi Yerusalemu adzachedwa, Madzi wa coonadi; ndi phiri la Yehova wa makamu, Phiri lopatulika.