12. Inde, anasanduliza mitima yao ikhale ngati mwala woti gwa, kuti angamve cilamulo, ndi mau amene Yehova wa makamu anatumiza ndi Mzimu wace mwa aneneri oyamba aja; m'menemo munafuma mkwiyo waukuru wocokera kwa Yehova wa makamu.
13. Ndipo kunacitika, monga Iye anapfuula, koma iwo sanamvera; momwemo iwo adzapfuula, koma Ine sindidzamva, ati Yehova wa makamu;
14. koma ndidzawabalalitsa ndi kabvumvulu mwa amitundu onse amene sanawadziwa. Motero dziko linakhala bwinja, m'mbuyo mwao; palibe munthu wopitapo ndi kubwererako; pakuti adaika dziko lofunikalo labwinja.