Zekariya 6:14-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo akorona adzakhala wa Kelemu, ndi wa Tobiya, ndi wa Yedaya, ndi wa Keni mwana wa Zefaniya, akhale cikumbutso m'Kacisi wa Yehova.

15. Ndipo iwo akukhala kutari adzafika, nadzamanga ku Kacisi wa Yehova, ndipo inu mudzadziwa kuti Yehova wa makamu ananditumiza kwa inu. Ndipo ici cidzacitika ngati mudzamvera mwacangu mau a Yehova Mulungu wanu.

Zekariya 6