3. Ndipo anati kwa ine, Ili ndi temberero lirikuturukira pa dziko lonse; pakuti ali yense wakuba adzapitikitsidwa kuno monga mwa ili; ndi ali yense wakulumbira zonama adzapitikitsidwa kuno monga mwa ili.
4. Ndidzaliturutsa ili, ati Yehova wa makamu, ndipo lidzalowa m'nyumba ya wakuba, ndi m'nyumba ya iye wolumbira monama pa dzina langa; ndipo lidzakhala pakati pa nyumba yace, ndi kuitha pamodzi ndi mitengo yace ndi miyala yace.
5. Pamenepo mthenga wakulankhula ndi ine anaturuka, nati kwa ine, Kwezatu maso ako, nuone ngati nciani ici cirikuturukaci.
6. Ndipo ndinati, Nciani ici? Nati iye, Ici ndi efa alikuturuka. Natinso, Ici ndi maonekedwe ao m'dziko lonse;