Zekariya 3:8-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Tamvera tsono, Yoswa mkulu wa ansembe, iwe ndi anzako akukhala pansi pamaso pako; pakuti iwo ndiwo cizindikilo; pakuti taonani, ndidzafikitsa mtumiki wanga, ndiye Mphukira.

9. Pakuti taona, mwalawo ndinauika pamaso pa Yoswa; pa mwala umodzi pali maso asanu ndi awiri; taonani, ndidzaloca malocedwe ace, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzacotsa mphulupulu ya dziko lija tsiku limodzi.

10. Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, mudzaitanizana yense mnansi wace patsinde pa mpesa ndi patsinde pa mkuyu.

Zekariya 3