1. Pamenepo anandionetsa Yoswa mkulu wa ansembe alikuima pamaso pa mthenga wa Yehova, ndi Satana alikuima pa dzanja lace lamanja, atsutsana naye.
2. Ndipo Yehova anati kwa Satana, Yehova akudzudzula, Satana iwe; inde Yehova amene anasankha Yerusalemu akudzudzula; uyu sindiye muuni wofumulidwa kumoto?
3. Koma Yoswa analikubvala nsaru zonyansa, naima pamaso pa mthenga.