4. nanena naye, Thamanga, lankhula ndi mnyamata uyu, ndi kuti, M'Yerusalemu mudzakhala anthu ngati m'midzi yopanda malinga, cifukwa ca kucuruka anthu ndi zoweta momwemo.
5. Pakuti Ine, ati Yehova, ndidzakhala kwa iye linga lamoto pozungulira pace, ndipo ndidzakhala ulemerero m'kati mwace.
6. Haya, haya, thawani ku dziko la kumpoto, ati Yehova; pakuti ndinakubalalitsani ngati mphepo zinai za kuthambo, ati Yehova.
7. Haya Ziyoni, thawa iwe wakukhala ndi mwana wamkazi wa Babulo.