13. Otsala a Israyeli sadzacita cosalungama, kapena kunena mabodza; ndi m'kamwa mwao simudzapezeka lilime lonyenga; pakuti adzadya nadzagona pansi, ndi palibe wakuwaopsa.
14. Yimba, mwana wamkazi wa Ziyoni; pfuula, Israyeli; kondwera nusekerere ndi mtima wonse, mwana wamkazi wa Yerusalemu.
15. Yehova wacotsa maweruzo ako, anataya kunja mdani wako; mfumu ya Israyeli, Yehova, ali pakati pako, sudzaopanso coipa.
16. Tsiku lomwelo adzati kwa Yerusalemu, Usaopa Ziyoni, manja anu asakhale olefuka.
17. Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi cimwemwe, adzakhala wopanda thamo m'cikondi cace; adzasekerera nawe ndi kuyimbirapo.
18. Ndidzasonkhanitsa iwo akulirira msonkhano woikika, ndiwo a mwa iwe, amene katundu wace anawakhalira mtonzo.