Zefaniya 2:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Dzisanthuleni, inde santhulani; inu mtundu wosakhumba kanthu;

2. lamulo lisanabale, tsiku lisanapitirire ngati mungu, usanakugwereni mkwiyo waukali wa Yehova, lisanakugwereni tsiku la mkwiyo wa Yehova.

3. Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m'dziko, amene munacita ciweruzo cace; funani cilungamo, funani cifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.

Zefaniya 2