9. Mulalikire ici mwa amitundu mukonzeretu nkhondo; utsani amuna amphamvu; amuna onse a nkhondo ayandikire nakwere.
10. Sulani makasu anu akhale malupanga, ndi anangwape anu akhale nthungo; wofoka anene, Ndine wamphamvu.
11. Fulumirani, idzani, amitundu inu nonse pozungulirapo; sonkhanani pamodzi, mutsitsire komweko amphamvu anu, Yehova.
12. Agalamuke amitundu, nakwerere ku cigwa ca Yosafati; pakuti ndidzakhala komweko kuweruza amitundu onse ozungulira,
13. Longani zenga, pakuti dzinthu dzaca; idzani, pondani, pakuti cadzala coponderamo mphesa; zosungiramo zisefuka; pakuti zoipa zao nzazikuru.
14. Aunyinji, aunyinji m'cigwa cotsirizira mlandu! pakuti layandikira tsiku la Yehova m'cigwacotsiriziramlandu.