Yoweli 2:20-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. koma ndidzakucotserani kutali nkhondo ya kumpoto, ndi kulingira ku dziko louma ndi lopasuka, a kumaso kwace ku nyanja ya kum'mawa, ndi a kumbuyo kwace ku nyanja ya kumadzulo; ndi kununkha kwace kudzakwera, ndi pfungo lace loipa lidzakwera; pakuti inacita zazikuru.

21. Usaopa, dziko iwe; kondwera, nusekerere; pakuti Yehova wacita zazikuru.

22. Musamaopa, nyama za kuthengo inu; pakuti m'cipululu muphukanso msipu; pakuti mitengo ibala zipatso zao; mikuyu ndi mipesa ipatsa mphamvu zao.

23. Mukondwere tsono, inu ana a Ziyoni, nimusekerere m'Yehova Mulungu wanu; pakuti adzayamba kukupatsani mvula yamyundo, monga mwa cilungamo cace; nakubvumbitsirani mvula, mvula yamyundo ndi yamasika mwezi woyamba.

24. Ndipo madwale adzakhala ndi tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; zidzasefuka m'zosungiramo zao.

Yoweli 2