Yoweli 1:18-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ha! nyama ziusa moyo, magulu a ng'ombe azimidwa; pakuti zisowa podyera; magulu a nkhosa omwe atha.

19. Ndipfuulira kwa Inu Yehova, pakuti moto wapsereza mabusa a m'cipululu, ndi malawi a moto anatentha mitengo yonse ya kuthengo,

20. inde nyama za kuthengo zilira kwa Inu; pakuti mitsinje yamadzi yaphwa, ndi moto wapsereza mabusa a m'cipululu.

Yoweli 1