Yoswa 6:26-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndipo Yoswa anawalumbirira nyengo ija, ndi kuti, Wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzauka ndi kumanga mudzi uwu wa Yeriko; adzamanga kuzika kwace ndi kutayapo mwana wace woyamba, nadzaimika zitseko zace ndi kutayapo mwana wace wotsirizira.

27. Potero Yehova anakhala ndi Yoswa; ndi mbiri yace inabuka m'dziko lonse.

Yoswa 6