13. Ndipo kunali, pokhala Yoswa ku Yeriko, anakweza maso ace, napenya, ndipo taona, panaima muthu pandunji pace ndi lupanga lace losolola m'dzanja lace; namuka Yoswa kuli iye, nati iye, Ubvomerezana ndi ife kapena ndi aelani athu?
14. Nati, lai, koma ndadza ine, kazembe wa ankhondo a Yehova. Pamenepo Yoswa anagwa nkhope yace pansi, napembedza, nati kwa iye, Anenanji Ambuyanga kwa mtumiki wace?
15. Ndipo kazembe wa ankhondo a Yehova anati kwa Yoswa, Bvula nsapato yako pa phazi lako; pakuti malo upondapo mpopatulika. Nacita Yoswa comweco.